Sukulu Yolepheleka

News reporter speaks

Mzanga yekhayo waku Chilinde
Anamubweza kugeli, fukwa fees sanalipire
Kwawo kunali kwa dolla, mdala yake isanatisiye
Ankala yekha achibale kunalibe
Ankaona mowa, chamba nzomwe zingamuthandize
Zachisoni pano analowa tchire
Mzanga wina anali waku Kawale
Sanali Yo, tinkamutcha mzimwale
Nthawi yadzinja ankatenga misale
Koma ana marra, sanamalize maphuzilo a sekondale
Waku Kaliyeka cha pa manda, mclass anali shasha
Panalibe babe yoti sinkamuwaza,onse anali nkhwanga, tinkamutcha shatta
Maths, Bio, zambiri sankatsata, Jokes yokhayo, class inkango khafa
Komwe anapita, palibe akudziwa
Tinangomva mbiri anapeleka mimba
Njira, ndizambiri m'mene sukulu imathela
Tsogolo lowala limalepheleka
Umphawi, imfa, ndi chibwana, zibwezi uli mwana
Izi ndi zina, zomwe zimachitika
Sisewelo, zimachitika
Ndizambiri zimachita, Sukulu umasiya
Ndizambiri zingachitike, Sukulu ndikusiya
Mzanga Limba, dolo kwambiri, wakutha kuyimba
Break yachiwiri, ayi sankafika
Aphuzitsi ankamulangiza, koma sankasintha
Mfana ovuta, chomwe ankafuna ndikutchuka
Notes analibe mclass ankamutulutsa
Lomwe anali nalo ndi kope lama rhymes
Tsiku lina sanabwele, two terms sanagele
Afuna amveke on made on Monday koma Joy sana player
Mpaka lero akupusha career
Nde kunali Maria, mkazi owala, ovuta kugwira
Mkazi odzimva, koma odziwa kutchila, number 1, pa top samatsika
Chosadziwa amayenda ndi sala
Anamupatsa phaa, pano amamwaso mankhwala
N'zake wa Jane, paja ndaa
Mmmh ndangoiwala dzina lake lenileni
Komwe ankakhala sanali abale ake eni eni
Ankamuzuza, ankamuuza mayeso sangakhoze, angozivutitsa
Nde sukulu anango dropa ndiku suntha, nkupeza mamuna
Adakatani, adasiya geli adakayifuna
Njira, ndizambiri m'mene sukulu imathela
Tsogolo lowala limalepheleka
Umphawi, imfa, ndi chibwana, zibwezi uli mwana
Izi ndi zina, zomwe zimachitika
Sisewelo, zimachitika
Ndizambiri zimachita, Sukulu umasiya
Ndizambiri zingachitike, Sukulu ndikusiya

Mother of child speaks to reporter



Credits
Lyrics powered by www.musixmatch.com

Link